Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:49 - Buku Lopatulika

49 Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana akazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 Ana aamuna a Saulo anali Yonatani, Isivi ndi Malikisuwa. Analinso ndi ana aŵiri aakazi, wamkulu anali Merabi, wamng'ono anali Mikala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 Ana aamuna a Sauli anali Yonatani, Isivi ndi Maliki-Suwa. Analinso ndi ana aakazi awiri, dzina la mwana wake wamkulu wamkazi linali Merabi ndipo la mwana wake wamngʼono wamkazi linali Mikala.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:49
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Saulo ndi ana ake, ndi Afilistiwo anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.


Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.


Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.


Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.


Chomwecho Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka.


Pakuti Saulo anapatsa Mikala, mwana wake, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi, wa ku Galimu.


Ndipo Afilisti anapirikitsa, osawaleka Saulo ndi ana ake; ndipo Afilisti anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa