Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:50 - Buku Lopatulika

50 ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

50 ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

50 Mkazi wa Saulo anali Ahinowamu mwana wa Ahimaazi. Ndipo mkulu wa ankhondo a Saulo anali Abinere, mwana wa Nere, mbale wa bambo wa Saulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

50 Dzina la mkazi wake linali Ahinoamu. Iyeyu anali mwana wa Ahimaazi. Dzina la mkulu wa ankhondo a Sauli linali Abineri mwana wa Neri, mʼbale wa abambo a Sauli.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:50
9 Mawu Ofanana  

Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwe kodi kuti kalonga ndi munthu womveka wagwa lero mu Israele?


Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide, Abinere analimbikira nyumba ya Saulo.


Ndipo zonse adazipatula Samuele mlauli, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndi Yowabu mwana wa Zeruya; aliyense anapatula kanthu kalikonse, anazisunga Selomoti ndi abale ake.


wa hafu la fuko la Manase mu Giliyadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yaasiyele mwana wa Abinere;


Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeze, tinadza kwa Samuele.


Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.


Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa