Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.
2 Samueli 23:1 - Buku Lopatulika Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa, Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Naŵa mau otsiriza a Davide: Nayi nyimbo ya Davide, mwana wa Yese, mau a munthu amene Mulungu adamkweza pamwamba, amene Mulungu wa Yakobe adamdzoza kuti akhale mfumu, munthu wokonda kuimba nyimbo zokoma za Israele: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nawa mawu otsiriza a Davide: “Mawu a Davide mwana wa Yese, mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba, munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo, woyimba nyimbo za Israeli: |
Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.
Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.
Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ochita ndiwo Asafu ndi abale ake.
Pakuti Davide yekha anena m'buku la Masalimo, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale padzanja langa lamanja,
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu ku Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana aamuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu.
Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani.
Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake.