Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 20:42 - Buku Lopatulika

42 Pakuti Davide yekha anena m'buku la Masalimo, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale padzanja langa lamanja,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Pakuti Davide yekha anena m'buku la Masalmo, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale pa dzanja langa lamanja,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Paja Davide yemwe m'buku la Masalimo akuti, “ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti: Khala ku dzanja langa lamanja

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 Davide mwini wake akunenetsa mʼbuku la Masalimo kuti, “Ambuye anati kwa Ambuye anga: ‘Khalani ku dzanja langa lamanja,

Onani mutuwo Koperani




Luka 20:42
12 Mawu Ofanana  

Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


kufikira Ine ndikaika adani ako pansi pa mapazi ako.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalimo, Pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wogonapo; ndipo uyang'aniro wake autenge wina.


Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.


Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?


Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa