Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 18:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Akaziwo ankapolokezana akukondwerera namati, “Saulo wapha zikwi inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Amayiwo ankalandizana nyimbo mokondwera namati: “Sauli wapha 1,000, Koma Davide wapha miyandamiyanda.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 18:7
8 Mawu Ofanana  

Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m'mzinda.


Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.


Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje.


Ndipo Miriyamu anawayankha, Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.


Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani?


Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.


Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa