1 Samueli 2:10 - Buku Lopatulika10 Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Chauta adzatswanya adani ake, adzaŵaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba. Chauta adzaŵaweruza mpaka ku mathero a dziko lapansi. Koma adzalimbikitsa mfumu yake, adzakuza mphamvu za wodzozedwa wake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Yehova adzaphwanya omutsutsa. Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba; Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi. “Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake, adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.” Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.