koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.
2 Samueli 22:8 - Buku Lopatulika Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko akumwamba adagwedezeka ndi kulilima chifukwa Chauta adaakalipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya. |
koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao.
Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.
Dziko lapansi linagwedezeka, inde thambo linakha pamaso pa Mulungu; Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israele.
Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.
Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;
Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Yehova, muja mudatuluka mu Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.