Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 77:18 - Buku Lopatulika

18 Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Phokoso la bingu lanu lidamveka konsekonse, mphezi zanu zidaŵalitsa dziko lonse, dziko lapansi lidanjenjemera ndi kugwedezeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu, mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 77:18
18 Mawu Ofanana  

Yehova anagunda kumwamba; ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ake.


Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.


Pa kudzudzula kwanu anathawa; anathawa msanga liu la bingu lanu;


Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa; inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.


Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi, nafukuka maziko a dziko lapansi, mwa kudzudzula kwanu, Yehova, mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.


Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.


Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu; dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.


Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.


Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika; anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m'dzanja lake, ndi komweko kunabisika mphamvu yake.


Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;


Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.


Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika mu Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukulu; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wake.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Yehova, muja mudatuluka mu Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa