Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 5:4 - Buku Lopatulika

4 Yehova, muja mudatuluka mu Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Yehova, muja mudatuluka m'Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 “Inu Chauta, pamene munkatuluka m'Seiri, pamene munkayenda kuchokera ku Edomu, dziko lidagwedezeka, kumlengalenga kudanjenjemera, mitambo idasungunuka nigwetsa madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri, pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu, dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka nigwetsa madzi.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 5:4
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino:


Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.


Amene agwedeza dziko lapansi lichoke m'malo mwake, ndi mizati yake injenjemere.


Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula, munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa.


Makongwa anatsanula madzi; thambo lidamvetsa liu lake; mivi yanu yomwe inatulukira.


Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.


Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulire konse, ngati iwo amene sanatchedwe dzina lanu.


Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang'ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetsereka.


Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala paphiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.


amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa