Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 22:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 “Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko akumwamba adagwedezeka ndi kulilima chifukwa Chauta adaakalipa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:8
13 Mawu Ofanana  

Aliyense amene wayikhudza mingayo amayidula pogwiritsa ntchito chigwandali kapena ndodo ya mkondo; nayitentha pa moto.”


Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera, ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.


Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, ndipo maziko a mapiri anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.


dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula, pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai. Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.


Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu, mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.


Njira yanu inadutsa pa nyanja, njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu, ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.


Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.


Mapiri amagwedera pamaso pake ndipo zitunda zimasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo.


Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika.


Kunachitika chivomerezi chachikulu, pakuti mngelo wa Ambuye anabwera kuchokera kumwamba ndipo anapita ku manda, nakagubuduza mwala nawukhalira.


Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.


“Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri, pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu, dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka nigwetsa madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa