Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
2 Samueli 22:11 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anaberekeka pa kerubi nauluka; inde anaoneka pa mapiko a mphepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anaberekeka pa kerubi nauluka; inde anaoneka pa mapiko a mphepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakwera pa mkerubi nauluka, adayenda mwaliŵiro ndi mphepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro. |
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.
Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.
Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ochokera kuchotetezerapo, pa mathungo ake awiri.
Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israele unakwera kuchoka pa kerubi, pamene unakhalira kunka kuchiundo cha nyumba, naitana munthu wovala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake.
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?
Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.