Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 104:3 - Buku Lopatulika

3 Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mwamanga Nyumba yanu pa madzi akumwamba, mitambo yaliŵiro ili ngati galeta lanu, mumayenda pa mapiko a mphepo,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake. Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake, ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 104:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anaberekeka pa kerubi nauluka; inde anaoneka pa mapiko a mphepo.


Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja;


Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.


Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.


ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake padziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.


Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.


Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe, wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza, ndi pa mitambo mu ukulu wake.


Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa