1 Samueli 4:4 - Buku Lopatulika4 Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Choncho adatuma anthu ku Silo kukatenga Bokosi lachipangano la Chauta Wamphamvuzonse wokhala pa akerubi. Ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, adapita nao pamodzi ndi Bokosi lachipanganolo ku zithando zankhondo zija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Choncho anatuma anthu ku Silo ndipo anakatenga Bokosi la Chipangano cha Yehova Wamphamvuzonse amene amakhala pa akerubi. Ndipo ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi anatsagana nalo Bokosi la Chipangano cha Mulungu. Onani mutuwo |