Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 4:5 - Buku Lopatulika

5 Pakufika likasalo la chipangano la Yehova kuzithando, Aisraele onse anafuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linachita chivomezi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakufika likasalo la chipangano la Yehova kuzithando, Aisraele onse anafuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linachita chivomezi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pamene Bokosi lachipangano la Chauta lidafika kuzithandoko, Aisraele onse adayamba kufuula kwambiri, kotero kuti nthaka idagwedezeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Bokosi la Chipangano cha Yehova litafika ku msasa, Aisraeli onse anafuwula kwambiri mpaka nthaka inagwedezeka.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:5
10 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mzindamo.


Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukulu, kotero kuti pansi panang'ambika ndi phokoso lao.


kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi?


Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa.


Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando wachiwawa;


Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake.


Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mzinda, yense kumaso kwake; nalanda mzindawo.


Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mzindawo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwake.


Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake.


Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa