1 Samueli 4:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Afilisti atamva phokoso la kufuulako adati, “Kodi kufuula kwakukulu kotere ku zithando za Ahebriku nkwa chiyani?” Atamva kuti Bokosi lachipangano la Chauta lafika kuzithandoko, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?” Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako, Onani mutuwo |