Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 4:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?” Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Afilisti atamva phokoso la kufuulako adati, “Kodi kufuula kwakukulu kotere ku zithando za Ahebriku nkwa chiyani?” Atamva kuti Bokosi lachipangano la Chauta lafika kuzithandoko,

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:6
4 Mawu Ofanana  

Tsono atsogoleri a Afilisti aja anafunsa kuti, “Kodi Ahebri awa akufuna chiyani?” Akisi anayankha kuti, “Uyu ndi Davide, mtumiki wa Sauli mfumu ya Israeli. Iye wakhala ndi ine kwa masiku ndithu, kapena titi zaka ndipo kuyambira tsiku limene anachoka kwa Sauli mpaka lero, ine sindinapeze cholakwa mwa iye.”


Bokosi la Chipangano cha Yehova litafika ku msasa, Aisraeli onse anafuwula kwambiri mpaka nthaka inagwedezeka.


Afilisti anachita mantha pakuti iwo ankanena kuti, “Milungu yafika ku msasa. Iwo anati, ‘Tili pamavuto. Chinthu choterechi sichinachitikepo nʼkale lomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa