1 Samueli 4:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Pamene magulu ankhondo adafika ku zithando, atsogoleri a Aisraele adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani Chauta walola kuti Afilisti atigonjetse? Tiyeni tikatenge Bokosi lachipangano la Chauta ku Silo, kuti Chautayo abwere pakati pathu ndipo atipulumutse kwa adani athu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Asilikali atabwerera ku misasa, akuluakulu a Israeli anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Yehova walola kuti tigonjetsedwe lero pamaso pa Afilisti? Tiyeni tikatenge Bokosi la Chipangano cha Yehova ku Silo kuti Yehovayo abwere kukhala pakati pathu ndi kutipulumutsa mʼmanja mwa adani athu.” Onani mutuwo |