Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 4:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Asilikali atabwerera ku misasa, akuluakulu a Israeli anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Yehova walola kuti tigonjetsedwe lero pamaso pa Afilisti? Tiyeni tikatenge Bokosi la Chipangano cha Yehova ku Silo kuti Yehovayo abwere kukhala pakati pathu ndi kutipulumutsa mʼmanja mwa adani athu.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamene magulu ankhondo adafika ku zithando, atsogoleri a Aisraele adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani Chauta walola kuti Afilisti atigonjetse? Tiyeni tikatenge Bokosi lachipangano la Chauta ku Silo, kuti Chautayo abwere pakati pathu ndipo atipulumutse kwa adani athu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 4:3
34 Mawu Ofanana  

Kenaka mfumu inati kwa Zadoki, “Tenga Bokosi la Mulungu ubwerere nalo mu mzinda. Ngati ndidzapeza chifundo pamaso pa Yehova, adzandibweretsa kuti ndilionenso ndi malo ake okhalamo.


Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”


Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?


Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja? Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!


Yehova akuti, “Kalata imene ndinasudzulira amayi anu ili kuti? Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole, ndinakugulitsani kwa ati? Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu; amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.


Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala kudya pamene Inu simukulabadirapo? Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa pamene Inu simunasamalepo?’ ” Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani, ndipo mumazunza antchito anu onse.


Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa, kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.


Koma zoyipa zanu zakulekanitsani ndi Mulungu wanu; ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu, kotero Iye sadzamva.


Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,” akutero Yehova.


Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’


Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo.


Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti, “Dzukani, Inu Yehova! Adani anu abalalike; Odana nanu athawe pamaso panu.


Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza.


Mitundu yonse ya anthu idzafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani Yehova anachita zotere mʼdziko lake? Kodi chifukwa chiyani anaonetsa mkwiyo woopsa wotere?”


“Tengani Buku ili la Malamulo ndi kuliyika pambali pa Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu. Likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani.


Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.


Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano.


Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’ ”


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anayitana ansembe ndipo anawawuza kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano cha Yehova ndipo ansembe asanu ndi awiri anyamule malipenga. Iwowa akhale patsogolo pake.”


Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani!


Tsono Ambuye, ine ndinene chiyani, pakuti tsopano Israeli anathamangitsidwa ndi adani ake?


Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha chikumbumtima choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu,


Ngakhale munazidziwa kale zonsezi, ndafuna kuti ndikukumbutseni kuti Ambuye anapulumutsa anthu ake ndi kuwatulutsa mʼdziko la Igupto, koma pambuyo pake anawononga amene sanakhulupirire.


Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo.


Tsono Sauli anawuza Ahiya kuti, “Bwera nalo Bokosi la Mulungulo.” (Nthawi imeneyo nʼkuti efodiyo ili ndi Ahiya pamaso pa Aisraeli).


Afilisti anandanda kuyangʼana Aisraeli nayamba kumenyana. Nkhondo inakula ndipo Afilisti anagonjetsa Aisraeli napha anthu 4,000 pa malo a nkhondopo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa