Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.
2 Samueli 19:27 - Buku Lopatulika Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu; chifukwa chake chitani chimene chikukomerani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Yehova; chifukwa chake chitani chimene chikukomerani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma iyeyo nkundisinjirira ine kapolo wanu kwa inu mbuyanga mfumu. Komatu inu muli ngati mngelo wa Mulungu. Nchifukwa chake tsono, muchite zimene zikukomereni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo wayankhula zosinjirira za ine mtumiki wanu kwa inu mbuye wanga mfumu. Mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu ndipo chitani chimene chikukomerani. |
Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.
Mnyamata wanu Yowabu anachita chinthu ichi kuti asandulize mamvekedwe a mlanduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse zili m'dziko lapansi.
Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.
Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.
Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.
Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.
Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake.
Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.
Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.
Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, Iye asamuke nafe kunkhondoko.