2 Samueli 19:28 - Buku Lopatulika28 Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201428 Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa28 Paja anthu onse a banja la bambo wanga anali oyenera kuphedwa ndi inu mbuyanga mfumu. Koma ine mtumiki wanu mudaandiika pakati pa anthu amene ankadya ndi inu pa tebulo lanu. Nanga ndingakhale ndi chiyaninso ine chimene chingandiyenereze kuti ndingadandaule kwa inu amfumu?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero28 Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?” Onani mutuwo |