Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Apo mfumu idati, “Basi ndamva usaonjezenso mau ena ai. Ine ndikufuna kuti iwe ndi Ziba mugaŵane chuma cha Saulo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:29
11 Mawu Ofanana  

Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?


Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.


Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Saulo dzina lake Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu amene.


Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.


Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Saulo, ninena naye, Za Saulo zonse ndi za nyumba yake yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako.


Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.


Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa?


Wobwezera mau asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.


koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa