Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 16:4 - Buku Lopatulika

4 Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Apo mfumu idauza Ziba kuti, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti nzako.” Ziba adati, “Pepani, ndakupembani, mbuyanga mfumu, bwanji nthaŵi zonse ndizipeza kuyanja pamaso panu!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndipo mfumu inati kwa Ziba, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako tsopano.” Ziba anati, “Ine modzichepetsa ndikukugwandirani, mbuye wanga mfumu, kuti ndipeze chisomo pamaso panu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 16:4
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yowabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yachita chopempha mnyamata wake.


Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.


Ndipo mfumu inanena ndi mkaziyo, Pita kunyumba yako, ndipo ndidzalamulira za iwe.


Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.


Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.


Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu; chifukwa chake chitani chimene chikukomerani.


Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.


Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Saulo, ninena naye, Za Saulo zonse ndi za nyumba yake yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako.


Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama.


Wobwezera mau asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.


Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama; koma mnzake afika namuululitsa zake zonse.


Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino; ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.


Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa