Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 16:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kenaka mfumu idamufunsa kuti, “Nanga mwana wa mbuyako ali kuti?” Ziba adayankha kuti, “Watsalira ku Yerusalemu, poti akunena kuti, ‘Aisraele andibwezera ufumu wa bambo wanga tsopano.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?” Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 16:3
13 Mawu Ofanana  

Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.


Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.


Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.


Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa, odziwana nane akhala kumdima.


Usamnamizire mnzako.


Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere; chilanda moyo wa eni ake.


Mboni yonama idzafa; koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika.


Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.


Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa