2 Samueli 16:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Mfumu idafunsa Ziba kuti, “Chifukwa chiyani wabwera ndi zimenezi?” Ziba adayankha kuti, “Amfumu, abuluŵa ndi oti anthu a m'banja mwanu azikwerapo. Bulediyu, ndi zipatso zapachilimwezi nzoti ankhondo azidya, ndipo thumba la vinyoli nloti anthu amene azikomoka m'chipululu azimwa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?” Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.” Onani mutuwo |