2 Samueli 16:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu paphiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao abulu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi nchinchi zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu pa phiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao abulu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi nchinchi zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Davide atabzola pang'ono pamwamba pa phiri, adakumana ndi Ziba, mtumiki wa Mefiboseti, ali ndi abulu a chishalo pa msana, atasenza buledi wokwanira 200, masangwe a mphesa 100, zipatso zapachilimwe 100, ndiponso thumba la vinyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo. Onani mutuwo |