Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 16:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu paphiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao abulu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi nchinchi zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu pa phiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao abulu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi nchinchi zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Davide atabzola pang'ono pamwamba pa phiri, adakumana ndi Ziba, mtumiki wa Mefiboseti, ali ndi abulu a chishalo pa msana, atasenza buledi wokwanira 200, masangwe a mphesa 100, zipatso zapachilimwe 100, ndiponso thumba la vinyo.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 16:1
17 Mawu Ofanana  

Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita.


Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe anthu ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki anadzakumana naye atangʼamba mkanjo wake ndi kudzithira fumbi kumutu.


Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu.


Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri.


Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli.


Mphatso ya munthu imamutsekulira njira yomufikitsa pamaso pa anthu akuluakulu.


Ine ndidzakhala ku Mizipa kuti ndizikuyimirirani kwa Ababuloni amene azidzabwera kwa ife, koma inu muzikolola vinyo wanu, zipatso zanu, mafuta anu ndi kuzisunga mʼmitsuko yanu, nʼkumakhala mʼmizinda imene mwalandayo.”


Tsono Ayuda onsewo anabwerera ku Yuda, ku Mizipa kwa Gedaliya, kuchokera ku mayiko onse kumene anabalalikira. Ndipo anakolola zipatso zochuluka ndi vinyo wambiri.


Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa.


Tsoka ine! Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe, pa nthawi yokolola mphesa; palibe phava lamphesa loti nʼkudya, palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.


“Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo.


Choncho Yese anatenga bulu namunyamulitsa buledi, thumba la vinyo ndi mwana wambuzi mmodzi. Zonsezi anamupatsa mwana wake Davide kuti akapereke kwa Sauli.


Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa