2 Samueli 16:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?” Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.” Onani mutuwoBuku Lopatulika2 Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Mfumu idafunsa Ziba kuti, “Chifukwa chiyani wabwera ndi zimenezi?” Ziba adayankha kuti, “Amfumu, abuluŵa ndi oti anthu a m'banja mwanu azikwerapo. Bulediyu, ndi zipatso zapachilimwezi nzoti ankhondo azidya, ndipo thumba la vinyoli nloti anthu amene azikomoka m'chipululu azimwa.” Onani mutuwo |