Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira bulu kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndili wopunduka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira bulu kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndili wopunduka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Mefiboseti adayankha kuti, “Ine mbuyanga mfumu, adaandilakwitsa ndi wantchito wanga. Kapolo wanune wantchitoyo ndidamuuza bwinobwino kuti, ‘Undimangire chishalo pa bulu kuti ndikwere, ndipite nawo limodzi amfumu,’ poti paja ine kapolo wanu ndine wolumala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga mfumu, pakuti ine wantchito wanu ndine wolumala. Ndinati, ‘Andikonzere chishalo cha bulu wanga ndipo ndidzakwera kuti ndipite ndi mfumu.’ Koma Ziba wantchito wanga anandilakwitsa.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:26
4 Mawu Ofanana  

Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.


Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti.


Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa