Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a ku Benjamini. Zibanso mtumiki uja wa m'banja la Saulo, pamodzi ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndiponso antchito ake makumi aŵiri, adathamangira ku Yordani, nakafikako isanafike mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:17
8 Mawu Ofanana  

Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana.


Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.


Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera.


Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.


Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Saulo dzina lake Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu amene.


Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa