Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 19:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndipo adaolotsa onse a m'banja la mfumu, nachita zonse zokondweretsa mfumuyo. Tsono pamene mfumu Davide anali pafupi kuwoloka Yordani, Simei mwana wa Gera, adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumuyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna. Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu,

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 19:18
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.


Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu.


Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.


Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.


Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Saulo dzina lake Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu amene.


Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga, koma nyengo yao ikadakhala yosatha.


Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.


Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa