Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 9:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Apo mfumu idamufunsa kuti, “Kodi palibe wina aliyense wa pa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo monga momwe ndidalonjezera kwa Mulungu?” Ziba adayankha kuti, “Padakali mwana wamwamuna wa Yonatani. Iyeyo ngwopunduka miyendo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?” Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 9:3
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira bulu kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndili wopunduka.


Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu; chifukwa chake chitani chimene chikukomerani.


Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti.


Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.


Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.


Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.


Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.


Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa