2 Samueli 9:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?” Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.” Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Apo mfumu idamufunsa kuti, “Kodi palibe wina aliyense wa pa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo monga momwe ndidalonjezera kwa Mulungu?” Ziba adayankha kuti, “Padakali mwana wamwamuna wa Yonatani. Iyeyo ngwopunduka miyendo.” Onani mutuwo |
(Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti).