Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
2 Samueli 15:26 - Buku Lopatulika Koma Iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andichitire chimene chimkomera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andichitire chimene chimkomera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma akapanda kukondwera nane, chabwino, andichite zomwe zimkomere.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma iye anati, ‘Akapanda kukondwera nane,’ chabwino, andichite chimene chimukomere.” |
Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.
Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?
Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo.
Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo.
Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.
Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?
Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
Ndipo tsopano, taonani, tili m'dzanja lanu; monga muyesa chokoma ndi choyenera kutichitira ife, chitani.
Koma ana a Israele anati kwa Yehova, Tachimwa, mutichitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani.
Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.