2 Samueli 11:27 - Buku Lopatulika27 Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Mkaziyo atatha kulira malirowo, Davide adatuma munthu nakamtenga, nkubwera naye kunyumba kwa mfumu, ndipo Davide adamukwatira. Mkaziyo adambalira mwana wamwamuna. Koma zimene adachita Davidezi zidaipira Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo. Onani mutuwo |