Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 12:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Mu mzinda wina munali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Pa mudzi wina panali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake Chauta adatuma mneneri Natani kwa Davide. Natani atafika kwa Davide, adamphera fanizo lakuti, “Mu mzinda wina munali anthu aŵiri, wina wolemera, wina wosauka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 12:1
24 Mawu Ofanana  

Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere.


Wolemerayo anali nazo zoweta zazing'ono ndi zazikulu zambiri ndithu;


Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


Monga mwa mau onse awa ndi monga mwa masomphenya onse awa, momwemo Natani analankhula ndi Davide.


Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.


Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.


Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya chaka chachitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.


Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israele, akhala mu Samariya; taona, ali ku munda wampesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira.


ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,


Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni?


Zochita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samuele mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli;


Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo achokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo achokera ku dziko lakutali, kudza kwa ine, kunena ku Babiloni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa