Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumzinda mumtendere pamodzi ndi ana ako aamuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumudzi mumtendere pamodzi ndi ana ako amuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Ndipo mfumuyo idauzanso Zadoki wansembe uja kuti, “Bwerera ku mzinda mwamtendere, iwe pamodzi ndi Abiyatara, ndi ana anu aŵiri, mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Mfumu inatinso kwa wansembe Zadoki, “Kodi siwe mlosi? Bwerera mu mzinda mwamtendere pamodzi ndi mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiatara. Iwe ndi Abiatara tengani ana anu awiri.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:27
11 Mawu Ofanana  

koma ukabwerera kumzinda, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele.


Onani, ali nao komweko ana aamuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze chilichonse mudzachimva.


Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mzinda.


Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera chilango adani ake.


Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,


Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.


Ahimaazi ku Nafutali, iyeyu adakwatira Basemati mwana wa Solomoni;


awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yake. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna khumi ndi anai, ndi ana aakazi atatu.


ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Ahimaazi,


Koma ananena naye, Onatu, m'mzinda muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.


Kale mu Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa