1 Mafumu 10:9 - Buku Lopatulika9 Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando waufumu wa dziko la Israele. Chifukwa choti Chauta adakonda Israele mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.” Onani mutuwo |