Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 39:9 - Buku Lopatulika

9 Ndinakhala duu, sindinatsegule pakamwa panga; chifukwa inu mudachichita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndinakhala duu, sindinatsegula pakamwa panga; chifukwa inu mudachichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndine mbeŵeŵe, sinditsekula pakamwa panga, pakuti ndinu amene mwachita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 39:9
8 Mawu Ofanana  

Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji?


nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova.


Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.


Koma ine, monga gonthi, sindimva; ndipo monga munthu wosalankhula, sinditsegula pakamwa panga.


ndi okhala padziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala padziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.


Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa