Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 39:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse, musandiike ndikhale chotonza cha wopusa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse, musandiike ndikhale chotonza cha wopusa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse. Musandisandutse chinthu chochinyodola zitsiru.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse; musandisandutse chonyozeka kwa opusa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 39:8
19 Mawu Ofanana  

Mundipatutsire chotonza changa ndichiopacho; popeza maweruzo anu ndi okoma.


Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.


Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse.


Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.


Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga; ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.


Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao; nati, Hede, Hede, diso lathu lidachipenya.


Mutisandutsa chotonza kwa anzathu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.


Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.


Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.


Mphulupulu zinandipambana; koma mudzafafaniza zolakwa zathu.


Takhala chotonza cha anansi athu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.


Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao?


Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu;


Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.


Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao.


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa