Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 39:10 - Buku Lopatulika

10 Mundichotsere chovutitsa chanu; pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Mundichotsere chovutitsa chanu; pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 “Chotsani chikoti chanu pa ine, ndatheratu chifukwa cha mkwapulo wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine; ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 39:10
10 Mawu Ofanana  

Mundichotsere dzanja lanu kutali, ndi kuopsa kwanu kusandichititse mantha.


Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.


Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe?


Andichotsere ndodo yake, choopsa chake chisandichititse mantha;


Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.


Akhale pa yekha, natonthole, pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete.


Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa