Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere.
2 Samueli 14:14 - Buku Lopatulika Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sakhoza kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja madzi akatayika saoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike, tsono amakonza njira yakuti wopirikitsidwa asakhale wotayikiratu chonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma poti madzi akatayika sawoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike kotero anakonza njira yakuti wopirikitsidwayo asakhale wotayikiratu. |
Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere.
Chifukwa chake tsono chakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndicho kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzachita chopempha mdzakazi wake.
Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.
Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.
Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi? Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse?
Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.
Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye.
Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.
Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?
Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,
Mizinda isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko.
ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumzinda wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.
popeza wakupha munthu akadakhala m'mzinda wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.
Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu.
Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho;
Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.
Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu;