Numeri 35:15 - Buku Lopatulika15 Mizinda isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Mizinda isanu ndi umodziyo idzakhala yothaŵirako Aisraele, alendo ndi anthu okhala pakati pao, kuti wina aliyense wopha munthu mnzake mwangozi azithaŵirako. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Midzi isanu ndi umodzi idzakhala malo opulumukirako Aisraeli, alendo ndi anthu ena onse okhala pakati pawo kuti wina aliyense wopha mnzake mwangozi adzathawireko. Onani mutuwo |