Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 11:25 - Buku Lopatulika

25 Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamudzipo, nuupasule; numlimbikitse motere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 11:25
8 Mawu Ofanana  

Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.


Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake.


Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mzinda wachifumu.


Koma anthu, ndiwo amuna a Israele, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.


Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa