Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 35:25 - Buku Lopatulika

25 ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumzinda wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumudzi wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Mpingo umpulumutse munthu wopha mnzakeyo m'manja mwa mbale wa munthu wakufayo. Ndipo um'bweze munthuyo ku mzinda wake wothaŵirako kumene adathaŵira. Adzakhala komweko mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Gulu lidzapulumutsa munthu wakuphayo mʼmanja mwa wolipsira uja ndi kumubwezera ku mzinda wopulumukirako kumene anathawira. Ayenera kukhala kumeneko kufikira imfa ya mkulu wa ansembe, amene anadzozedwa ndi mafuta oyera.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:25
15 Mawu Ofanana  

Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza.


Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung'amba zovala zake.


akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.


Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.


pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzakeyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;


Koma wakupha munthu akatuluka nthawi iliyonse kulumpha malire a mzinda wake wopulumukirako kumene anathawirako;


popeza wakupha munthu akadakhala m'mzinda wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.


Ndipo azikhala m'mzindamo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumzinda kwake, ndi nyumba yake, kumzinda kumene adathawako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa