Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 9:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Amoyo amadziŵa kuti adzafa, koma akufa sadziŵa kanthu, ndipo alibe mphotho inanso yoonjezera. Palibe ndi mmodzi yemwe woŵakumbukira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa kanthu; alibe mphotho ina yowonjezera, ndipo palibe amene amawakumbukira.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 9:5
18 Mawu Ofanana  

Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sangathe kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.


Ana ake aona ulemu osadziwa iye; napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.


Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa, ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse.


Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire, kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi.


Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu; m'mandamo adzakuyamikani ndani?


Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova, ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa.


Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.


Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.


Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.


Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumzinda nawaiwala; ichinso ndi chabe.


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali nacho chiyembekezo; pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa.


Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; chifukwa chake Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa chikumbukiro chao chonse.


Pakuti Inu ndinu Atate wathu, ngakhale Abrahamu satidziwa ife, ndi Israele satizindikira ife. Inu Yehova ndinu Atate wathu, Mombolo wathu wachikhalire ndi dzina lanu.


Pomalizira anamwaliranso mkaziyo.


Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa