Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.
2 Akorinto 3:12 - Buku Lopatulika Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popeza kuti timayembekeza zimenezi, timalimba mtima kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri. |
Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.
Ophunzira ake ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena chiphiphiritso.
Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao.
Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.
Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti mu Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.
koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;
Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala mu ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili mu ulemerero.
Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula;
Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.
ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.
monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.
koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.
Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu mu Khristu kukulamulira chimene chiyenera,