Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 16:25 - Buku Lopatulika

25 Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 “Ndakuuzani zimenezi mophiphiritsa. Nthaŵi ilikudza pamene sindidzalankhula nanunso mophiphiritsa, koma ndidzakudziŵitsani momveka za Atate.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 “Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 16:25
19 Mawu Ofanana  

Ndidzatchera khutu kufanizo, ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira.


Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira; ndidzatchula zinsinsi zoyambira kale.


kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake, mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao.


Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu.


Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse?


ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.


Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula.


Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.


Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikire zimene Yesu analikulankhula nao.


Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,


koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa