Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:29 - Buku Lopatulika

29 ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Ankalankhulanso ndi kumatsutsana ndi Ayuda olankhula Chigriki, koma iwowo ankafunafuna kumupha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Anayankhula ndi kutsutsana ndi Ayuda a Chihelene, koma iwo ankafuna kumupha.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:29
13 Mawu Ofanana  

Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu.


Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.


Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.


ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga mu Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.


Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku.


Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti mu Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.


Ndipo anali pamodzi nao, nalowa natuluka ku Yerusalemu, nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye;


paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mzinda, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga;


Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.


Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbike mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa