Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 9:27 - Buku Lopatulika

27 Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti mu Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Pamenepo munthu wina, dzina lake Barnabasi, adamtenga napita naye kwa atumwi. Iye adaŵafotokozera za m'mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja, ndipo kuti Ambuye adaalankhula naye. Adaŵasimbiranso za m'mene Saulo ku Damasiko ankalankhulira molimba mtima m'dzina la Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Koma Barnaba anamutenga napita naye kwa atumwi. Iye anawafotokozera iwo za mmene Saulo anaonera Ambuye pa njira paja, ndi kuti Ambuye anamuyankhula, ndi momwe analalikira ku Damasiko mʼdzina la Yesu mosaopa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 9:27
20 Mawu Ofanana  

Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala mu Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya;


Ndipo anatuluka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo;


Ndipo Barnabasi ndi Saulo anabwera kuchokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo.


Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.


Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,


Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnabasi (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kipro,


Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani panjira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.


ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye.


ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.


Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito?


Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.


ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa