Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 7:4 - Buku Lopatulika

4 Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndimakukhulupirirani kwambiri, ndipo ndimakunyadirani kwenikweni. Zondilimbitsa mtima zandichulukira, ndipo m'zovuta zathu zonse ndakondwa kopambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ndimakukhulupirirani kwambiri ndipo ndimakunyadirani kwambiri. Ndikulimbikitsidwa kwambiri; mʼmasautso athu onse, chimwemwe changa chilibe malire.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 7:4
27 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu a milandu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.


Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;


Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chinapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu;


monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.


wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.


Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;


Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.


Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.


Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu,


Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.


Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.


ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.


monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.


kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke mu Khristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.


Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;


Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;


Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwake?


koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu mu Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;


Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.


Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa